ad

Namwino Wachinyengo Apereka Chindaputsa

Star InactiveStar InactiveStar InactiveStar InactiveStar Inactive
 

Mtsikana wa zaka 22, Caroline Botha, yemwe anamangidwa kaamba konamiza anthu kuti iye ndi namwino komanso kubera odwala pa chipatala cha Area 25 mu mzinda wa Lilongwe amulamula kupereka chindaputsa cha ndalama zokwana 90 thousand kwacha.

Bwalo la Mkukula First Grade m’boma la Dowa kudzera mwa Oyimira boma pa mlandu, Jolly Kamazulu, linamvua kuti Caroline Botha anapalamula mlandu-u pa 7 September.

Malingana ndi Kamazulu, opalamula-yu yemwe ali ndi certificate ya MSCE,  wakhala akumapita pa chipatalapa atamvala ngati namwino kenako kumabwereka ndalama kwa odwala powanamiza kuti akulu-akulu apa chipatalapa ndi omwe abweze ndalamazo.

Caroline Banda anavomera mlandu-u ndipo anapempha bwalo la Milandu kuti limukhululukire ponena kuti wachimina ndipo sazayambiranso.

Popereka chigamulo chake Oweruza mlandu Thomson Midias analamula Caroline Banda kupereka chindaputsa cha ndalama zokwana 90 Thousand komanso kuti asapalamulenso mlandu onga omwewu kwa chaka ndi miyezi 6.

Follow Us

Popular Post

Remove Children From Streets Or Risk Arrest – Kaliati

Malawi News Agency Sep 30, 2021 NATIONAL NEWS

By Andrew Magombo Minister of Gender, Community Development and Social Welfare, Patricia Kaliati, has issued a two-week ultimatum to irresponsible pa...