ad

Kusowekera kwa Madzi A Ukhondo Kwafika Posawuzana Ku Bangwe

Star InactiveStar InactiveStar InactiveStar InactiveStar Inactive
 

Pali nkhawa kuti anthu ena okhala ku Bangwe mu mzinda wa Blantyre ali pa chiopsezo chodwala matenda odza kaamba kakusowa kwa madzi a ukhondo pomwe zadziwika kuti madzi a m’mipopi komanso mijigo ndi zosakwanira mderali.

Vutoli akuti likuikanso pa chiopsezo chitetezo cha amai omwe amalawilira m’mawa kwambiri kukafuna-funa madzi m’madera akutali.

Ndirande FM itayankhula ndi anthu ena mwa amai-wa, zadziwika kuti amakumana ndi anthu ena omwe amatha kuwachita chipongwe, zinthu zomwe zimawachititsa kuti aziyenda a mantha.

Mai Caroline Chatha omwe ndi m’modzi mwa amai-wa ati vuto la kusowa kwa madzi likukulira-kulira mu nyengo ino ya chilimwe pomwe zitsime zomwe amadalira zikuuma.

Ndipo oyang’naira za umoyo ndi ukhondo wa anthu ku Bangwe, Jane Matewere wati izi zikukhuza ntchito yolimbikitsa ukhondo mderali.

Pakadali pano, mai Matewere apempha adindo kuti achitapo kanthu mwachangu.

Mneneri wa bungwe lopopa ndi kugulitsa madzi mu mzinda wa Blantyre la Blantyre Water Board (BWB), Evelyn Khonje sanayankhe lamya yake ya m’manja titamuimbira kangapo konse ndi cholinga choti afotokozere zomwe bungwe likuchita pothana ndi vutoli.

Pa nkhani ngati yomweyi, Zadziwika kuti chipatala cha Mpherembe chomwe chili m’boma la Mzimba chakhala opanda madzi a pa mpopi pafupi-fupi kwa miyezi inayi tsopano zomwe zikuika odwala komanso ogwira ntchito pa chipatala-pa pa chiwopyezo.

Malingana ndi Malawi News Agency, mpopi komanso njingo zomwe zinali pa malopa zinawongeka ndipo adindo sakuwonetsa chidwi chili chonse chofuna kukonza zinthu-zi pa malopa.

Wa pa Mpando wa Komiti ya chitukuko ya Mpherembe, a Bruce Lungu, wadzuzula adindo kaamba kolekelera zinthu pa chipatalapa pomwe wati zomvesa chisoni kuti chipatala-chi chakhala opanda madzi kuyambira mwezi wa June.

A Lungu awonjezera kunena kuti kangapo konse akhala akupita kukanena za vutoli ku ofesi ya ofesi ya za umoyo koma akulu akulu ku ofesi-yi amangoleza kuti akonza vutoli uku ma tsiku kumapita.

Koma m’modzi mwa akulu akulu ku Khonsolo ya m’boma la Mzimba, a Tamara Nyirongo, wati akambirana ndi ofesi ya za umoyo m’derali kuti apeze njira yothana ndi vutoli mwa msanga.

Follow Us

Popular Post

Remove Children From Streets Or Risk Arrest – Kaliati

Malawi News Agency Sep 30, 2021 NATIONAL NEWS

By Andrew Magombo Minister of Gender, Community Development and Social Welfare, Patricia Kaliati, has issued a two-week ultimatum to irresponsible pa...