ad

'Chakwera Sanatsate Malamulo Pobwezeletsa Mfumu Yaikulu Ngabu'

Star InactiveStar InactiveStar InactiveStar InactiveStar Inactive
 

Bwalo la High Court mu mzinda wa Blantyre lati President Lazarus Chakwera anaphwanya malamulo pobwezeletsa pa mpando Noah Dalasi ngati mfumu yaikulu Ngabu ya m’boma la Chikwawa.

Oweruza mlandu Justice Mandala Mambulatsa ndi yemwe wapereka chigamulochi lero la Chiwiri ponena kuti kubwezeletsedwa kwa a Dalasi kunali kotsatsata malamulo a dziko lino.

Justice Mandala Mambulatsa walamulanso President Lazarus Chakwera apereke ndalama zonse zomwe zagwilitsidwa ndi mbari yodandaula pa mlandu-u, zomwe ndikuphatikiza zolipilira ma Lawyer.

Chigamulochi chaperekedwa bambo Basitole Dalison Makwalu, omwe anasakhidwa kuti alowe m’malo mwa mfumu Yaikulu Ngabu atakamang’ara ku bwalo kusatira kubwezeretsedwa pa Mpando kwa a Dalasi ndi President Chakwera.

A Dalasi anachotsedwa ngati mfumu yaikulu Ngabu pa 12 December 2019 ndi yemwe anali President wa dziko lino a Peter Mutharika, poyiganizira kuti imakhuzidwa ndi nkhani za katangale.

Follow Us

Popular Post

Remove Children From Streets Or Risk Arrest – Kaliati

Malawi News Agency Sep 30, 2021 NATIONAL NEWS

By Andrew Magombo Minister of Gender, Community Development and Social Welfare, Patricia Kaliati, has issued a two-week ultimatum to irresponsible pa...