ad

Apolisi Amanga Apolisi Ku Lilongwe

Star InactiveStar InactiveStar InactiveStar InactiveStar Inactive
 

Apolisi m’dziko muno amanga apolisi amnzawo okwana awiri komanso anthu ena okwana atatu omwe amagwira ntchito ku nthambi ina ya boma powaganizira kuti akhala akupanga kalata za chinyengo zomwe amazigwiritsa ntchito pokuba ndalama za misonkho

Malingana ndi mneneri wa apolisi m’dziko muno, James Kadazera, kafuku-fuku wa polisi akuonetsa kuti izi zakhala zikuchitika kuyambira m’mwezi wa July chaka chatha kufika m’mwezi wa June chaka chino pomwe ndalama zopitilira 14 million kwacha zinabedwa kudzera mu njirayi.

Omangidwawa ndi a Victor Masonga omwe ndi apolisi, a Emmanuel Magombo, apolisi-nso, a Philip Mwenye komanso Theresa Nkhoma omwe ndi a ku nthambi yoona zotsindikiza kalata ku m’boma ndipo onse ali ndi zaka 46 zakubadwa komanso a Dennis Banda a zaka 58 omwe amagwiranso ku nthambi yotsindikiza kalatayi.

 A Kadazera ati anthu-wa awatengera ku bwalo la milandu posachedwapa ndipo akawatsegulira milandu yopanga kalata za chinyengo komanso kuba ndalama za boma mwa ina.

Follow Us

Popular Post

Remove Children From Streets Or Risk Arrest – Kaliati

Malawi News Agency Sep 30, 2021 NATIONAL NEWS

By Andrew Magombo Minister of Gender, Community Development and Social Welfare, Patricia Kaliati, has issued a two-week ultimatum to irresponsible pa...